STAY ALIVE Initiative

STAY ALIVE Initiative Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from STAY ALIVE Initiative, Mental Health Service, Blantyre.

UTHENGA WOCHOKERA KU STAY ALIVE INITIATIVETikhala tikudziwitsani kuti abambo okwana 125 adzipha kuyambira January mpaka ...
27/04/2025

UTHENGA WOCHOKERA KU STAY ALIVE INITIATIVE

Tikhala tikudziwitsani kuti abambo okwana 125 adzipha kuyambira January mpaka March chaka chino. Chiwerengerochi ndichokwera poyerekeza ndi abambo 109 omwe adzipha pa nthawi yomweyi chaka chatha.

Malinga ndi zomwe wachiwiri kwa M'neneri wa Apolisi, a Harry Namwaza, adafotokozera, zinthu monga ngongole, mavuto a m’banja komanso kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo ndi zomwe zikuchititsa anthu ambiri kudzipha.

Pakadali pano, anthu onse omwe adzipha chaka chino ndi 153 – abambo 125 ndi amayi 28.

Tikupempha abambo onse komanso aliyense amene akukumana ndi mavuto kuti asamadziphimbe ndi nkhawa. Funsani thandizo! Limbikitsani kutuluka poyankhula ndi anzanu kapena kupita kwa maofesi a Apolisi omwe ali pafupi nanu kuti mupeze chithandizo choyenera.
Moyo ndi wofunika – tiyeni tikhale ndi moyo!

Stay Alive Initiative – Kukuthandizani Kukhalabe ndi Moyo.

Warmest wishes from Stay Alive Initiative! 🤗 Eid Mubarak to all Muslims around the World! 🌎🕊️ May this blessed occasion ...
31/03/2025

Warmest wishes from Stay Alive Initiative! 🤗 Eid Mubarak to all Muslims around the World! 🌎🕊️ May this blessed occasion bring peace, 🕊️ joy, 🎉 and happiness to you and your loved ones. 🌈❤️ 💖.

WAZIPHA NDIPO WASIYA KALATA IYI KU NSANJE💔😢Uyu ndi mnyamata wachichepere kwambiri yemwe wazipha pokumwa mankhwala. Dzina...
08/02/2025

WAZIPHA NDIPO WASIYA KALATA IYI KU NSANJE💔😢

Uyu ndi mnyamata wachichepere kwambiri yemwe wazipha pokumwa mankhwala. Dzina lake ndi Yamikan Junior Thom ochokera kwa Sorgin-Nsanje yemwe amagwira ntchito ngat Agent wa Airtel money ndi mpamba pa stage ya sorgin yopita ku Blantyre. Iye wasiya chibaluwa chomwe chikufotokoza chifukwa chomwe waziphera.

Kwa omwe sitikwanitsa kuona zolembazi alemba kuti" Pepani pepani panalibe kuchitila mwina koma ndinayesetsa ndakanika ngati kungakhale kotheka tidzakumana. Anthu ndili nawo ngongole zawo zambiri,mupange black card yanga ya airtel 0984735183 muli ndalama zambiri pin ndi 2000.

Anzamga nonse ndikusowani ndafera kusaka" uwu nd uthenga wasiya Thom.

Chonde achinyamata kuzipha si solution pezan chithandizo ndi maganizo kwa anzathu osat kuzipha . R I P.

Ngati inu kapena wina amene mukumudziwa akufunika thandizo la maganizo, chonde fikirani ku page iyi. Tikhalebe ndi moyo ndi kuthandizana wina ndi mnzake!.Mzimu wa Jofilisi ukause mumtendere 💔 💔

Plz follow STAY ALIVE Initiative


゚viralシ2024fyp

😭💔 Tragic Story! 💔😭A man took his own life when he discovered the child he raised wasn't his. Now, his wife is left alon...
08/02/2025

😭💔 Tragic Story! 💔😭

A man took his own life when he discovered the child he raised wasn't his. Now, his wife is left alone, walking around him, and he's no longer there to wonder... "Are there no good women in the world?" 😭

This story is a sad reminder that life can be tough and unexpected. But we must remember that WE ARE NOT ALONE! 🌎

If you're feeling overwhelmed, lost, or struggling, PLEASE REACH OUT! 🤗 Talk to someone, share your feelings, and know that there's help available. 🌈

Let's break the silence and support each other. You are NOT alone, and there IS hope! 💕

Stay Alive, Stay Strong! 🌟

💖

Nkhani yomvetsa Chisoni.😢💔Padakali pano munthu yemwe wazipha pa Manda apa Biwi sakudziwika, ndiye mwina mukhoza kuwazind...
08/02/2025

Nkhani yomvetsa Chisoni.😢💔

Padakali pano munthu yemwe wazipha pa Manda apa Biwi sakudziwika, ndiye mwina mukhoza kuwazindikira nkhope..

Ngati inu kapena wina amene mukumudziwa akufunika thandizo la maganizo, chonde fikirani ku page iyi. Tikhalebe ndi moyo ndi kuthandizana wina ndi mnzake!.Mzimu wa Jofilisi ukause mumtendere 💔 💔

Plz follow STAY ALIVE Initiative


゚viralシ2024fyp


WAZIPHA KU JONI MDZIKO LA SOUTH AFRICA 💔 M'nyamata otchedwa Chombe Jofilisi wa mmudzi  wa mfumu Mkuziwaduka,TA Mgabu  m'...
08/02/2025

WAZIPHA KU JONI MDZIKO LA SOUTH AFRICA 💔

M'nyamata otchedwa Chombe Jofilisi wa mmudzi wa mfumu Mkuziwaduka,TA Mgabu m'boma la Nsanje wamwalira pozikhweza ndi chingwe mdziko la South Africa.

Malinga ndi amene amakhala ndi malemu Jofilisi,akuti iyeyu wazimangilira pa ntchire, dzana masana ku malo otchedwa Stanger mdzikolo, potsatira mavuto omwe amakomana nao komanso kusowa kwa chisamaliro kuchokera kwa abale ake.

Mwa zina malemu Jofilisi akuti wafika ku south Africa ma week atatu apitawa kuchokera ku Mozambique komwe wakhala mmanja mwa a police pafupi fupi miyezi itatu kamba kosowa ziphatso zoyendera ( Passport).

Ngati inu kapena wina amene mukumudziwa akufunika thandizo la maganizo, chonde fikirani ku page iyi. Tikhalebe ndi moyo ndi kuthandizana wina ndi mnzake!.Mzimu wa Jofilisi ukause mumtendere 💔 💔

Plz follow @


゚viralシ2024fyp

  Bambo wina wamwalira atadzimangilira m'nkhalango ya bungwe logawa madzi ya Central Region Water Board komwenso kuli Da...
18/01/2025



Bambo wina wamwalira atadzimangilira m'nkhalango ya bungwe logawa madzi ya Central Region Water Board komwenso kuli Dam m'boma la Kasungu.

Apolisi atafika pa malowa panali kusamvana ndi anthu ogwira ntchito ku bungweri kamba ka ganizo la apolisiwo kuti ayike ntembowo m'nkhalango momwemo ponena kuti lawonongeka kwambiri.

Komabe apolisiwa ngakhale anatero adindo ku bungweri anakana zomwe zinapangitsa apolisi kuchoka pa malopo.

M'modzi mwa anthu omwe anali pa malowa a Isaac Daka anati munthuyo akuwoneka kuti anafa masiku angapo apitawo ponena kuti thupi lake linayamba kuwonongeka komanso limatulutsa fungo.

Pakanali pano anthu ogwira ntchito ku bungweri anyamula thupilo ndipo ati aliyika m'manda a kwa Juma m'boma lomweri la Kasungu.

Osayiwala follow 👉 SSTAY ALIVE Initiative

WAZIPHA KAMBA KA MAVUTO💔😭Yamikani Khifra akwa T/A Nkanda ku Mchinji wazipha kamba ka mavuto omwe akhala akumana nawo.Khi...
14/01/2025

WAZIPHA KAMBA KA MAVUTO💔😭

Yamikani Khifra akwa T/A Nkanda ku Mchinji wazipha kamba ka mavuto omwe akhala akumana nawo.

Khifra wapezeka mnyumba mwake atazimangilira ku Chipinda chomwe amagona.Mzimu wake ukause muntendere💔

Ngati inu kapena wina amene mukumudziwa akufunika thandizo la maganizo, chonde fikirani ku page iyi. Tikhalebe ndi moyo ndi kuthandizana wina ndi mnzake!.


゚viralシ2024fyp

14/01/2025



Ophunzira wa pa sukulu ya sekondale ya Chiradzulu CDSS, Shyreen Sowa wa zaka 17 wadzipha pa nkhani zokhudza chikondi.

Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali a Cosmas Kagulo wati malemuyu wachita izi bwenzi lake litamuuza kuti silikumufunanso.


゚viralシ2024fyp


RIP George😭 🕊️George wa ku Ekwendeni, Mzuzu, wadzipha atazindikira kuti chibwenzi chake chikumupanga cheat kumbali and a...
09/01/2025

RIP George😭 🕊️

George wa ku Ekwendeni, Mzuzu, wadzipha atazindikira kuti chibwenzi chake chikumupanga cheat kumbali and amapakulisa kwa munthu wina💔. Ngati mukuvutika, fikirani pulogalamu yathu ya Khala Alibe, muthandizidwa 🤝. 🌟 Simuli nokha 🌈

04/01/2025

UTHENGA WOFUNIKA KUCHOKERA KWA HABAKKUK 🌟

Onerani tsopano pamene Habakuku akugawana uthenga wa chiyembekezo ndi chilimbikitso, kutikumbutsa kusankha moyo ndi kupewa zoipa.Ndikukufunirani Chaka Chatsopano chosangalatsa komanso chodala kuchokera ku Stay Alive Initiative! 🎉🎉

Chaka Chabwino Chatsopano! 🎉 Chaka chanu chikhale chodzaza ndi chisangalalo & kumwetulira! 😊 Ikani patsogolo thanzi lanu...
01/01/2025

Chaka Chabwino Chatsopano! 🎉 Chaka chanu chikhale chodzaza ndi chisangalalo & kumwetulira! 😊 Ikani patsogolo thanzi lanu lamalingaliro & thanzi lanu mu 2025 🧠. Tiyeni tilimbane ndi nkhani zamisala limodzi! 💪


STAYSTAY ALIVE InitiativeToSuicide

Address

Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when STAY ALIVE Initiative posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share