Anaesthesia Association of Malawi

Anaesthesia Association of Malawi Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Anaesthesia Association of Malawi, Health & Wellness Website, P. O Box 95, Blantyre.

The Anaesthesia Association of Malawi (AAM) is a professional body representing anaesthesia providers in Malawi, including anaesthetists, clinical officers, and other practitioners involved in perioperative care and Intensive care Medicine in Malawi

KODI MUKUDZIWA?Chifukwa chiyani ogwira ntchito m’chipinda cha operation (Theatre) amavala ndikugwilitsa ntchito zovala k...
31/07/2026

KODI MUKUDZIWA?

Chifukwa chiyani ogwira ntchito m’chipinda cha operation (Theatre) amavala ndikugwilitsa ntchito zovala kapena nsalu za green kapena za blue ?

■Mitundu imeneyi imasankhidwa chifukwa cha science komanso kuthandiza gulu la anaesthesia ndi team yonse kugwira ntchito bwino.

🟢 Imachepetsa kutopa kwa maso:
Green ndi blue zimathandiza kuchepetsa kutopa kwa maso pambuyo poyang’ana kuwala kwa magetsi ambiri amu theatre,magazi ndi minofu kwa nthawi yayitali pa operation.

👁️ Imathandiza kuona kusintha kwa wodwala:
Kutha kuzindikira kusintha kwa khungu, milomo, magazi, ndi zizindikiro zina mwansanga. Anaesthetist ndi team yomwe ikupanga operation imatha kuwona mnsanga ngati odwala akutaya magazi or khungu lasintha colour

🧼 Ndi gawo la ukhondo ndi ukatswiri wa theatre:
Zovala, nsalu ndi ma gown ndi mbali ya malamulo a chitetezo cha wodwala komanso kasamalidwe ka malo a opaleshoni. Zimafunika kuvala zochapa ndi kuyeletsedwa bwino kusunga ukhondo

NOTE :
Zovala ndi nsalu za blue kapena green sizimasankhidwa chifukwa cha kukongola kokha. Ndi gawo la theatre environment lomwe limathandiza kuchepetsa kutopa kwa maso komanso kuthandiza gulu la opaleshoni kupereka chisamaliro chapamwamba.

💬 Kodi munali mukudziwa ? Like Share and Follow our page for more information



ANAESTHESIA AND INTENSIVE CARE MEDICINE SAFETY SERIESEvery Patient. Every Procedure. Every Time.🛡️ 1. PATIENT SAFETYPati...
29/07/2026

ANAESTHESIA AND INTENSIVE CARE MEDICINE SAFETY SERIES

Every Patient. Every Procedure. Every Time.

🛡️ 1. PATIENT SAFETY
Patient Safety Comes First Patient safety is at the heart of every anaesthetic. Vigilance, teamwork, and continuous monitoring save lives.
---
💉 2. DRUG LABELLING
Label It. Check It. Give It Safely. Every syringe must be clearly labelled and checked before administration.
---
🩺 3. PRE-OPERATIVE ASSESSMENT
Safety Begins Before Surgery. A thorough pre-operative assessment identifies risks and guides safe anaesthetic care.
---
⚙️ 4. ANAESTHETIC MACHINE CHECKS
Check the Machine Before Every Case. Always inspect the anaesthetic machine and equipment before use.
---
🏥 5. SAFE WORKING ENVIRONMENT
Safety Starts with the Team. A clean, organised theatre and effective teamwork reduce errors and improve patient outcomes.
---
📝 6. DOCUMENT FOR SAFETY
Document to be safe and protect .Accurate documentation improves communication, continuity of care, and patient safety.
---
🩹 7. ESSENTIAL EQUIPMENT
Be Prepared. Be Safe. Never begin anaesthesia without oxygen, suction, airway equipment, monitoring, emergency drugs, and resuscitation equipment.
---

🛡️ NOTE
Preparation. Vigilance. Teamwork = Safety.
Together, we deliver safe anaesthesia and better patient outcomes.




DZIWANI ZA MANKHWALA ATHU: KETAMINEMankhwala a anaesthesia othandiza kugona bwino kwa odwala pa nthawi ya opaleshoni kom...
28/07/2026

DZIWANI ZA MANKHWALA ATHU: KETAMINE

Mankhwala a anaesthesia othandiza kugona bwino kwa odwala pa nthawi ya opaleshoni komanso kuchepetsa ululu.

Anthu ena amaganiza kuti ketamine ndi mankhwala obwebwetesa kapena kuwulula zinsinsi , koma amenewa ndi maganizo olakwika. Ketamine ndi mankhwala a anaesthesia ochepetsa ululu omwe amagwiritsidwa ntchito ndi akatswiri azaumoyo pa maopaleshoni kapena pa ngozi komanso ndi malo osamalira anthu odwalika.

🔹 Ketamine amathandiza:
✅ Kugonetsa wodwala pa nthawi ya opaleshoni
✅ Kuchepetsa ululu
✅ Kuthandiza wodwala kusakumbukira njira yomwe yachitika komaso zomwe zimachitika pa opaleshoni

🔹 N’chifukwa chiyani Ketamine ali wapadera?
🫁 Amathandiza kupuma komanso kusunga ntchito ya mtima ndi magazi bwino.

🔹 N’chifukwa chiyani ena amamva ngati “abwebweta”?
Izi ndi zotsatira zakanthawi za mankhwalawa, monga maloto achilendo, Kuyankhula kwambiri kapena kusokonezeka munthu akadzuka.

Side Effects (Zotsatira Zoipa) za Ketamine
• Chizungulire (Dizziness)
• Kusanza kapena nseru (Nausea or vomiting)
• Kugona kwambiri (Excessive drowsiness)
• Kusokonezeka maganizo kapena ma hallucinations (Confusion or hallucinations)
• Kuthamanga kwa mtima ndi kukwera kwa BP (Increased heart rate and blood pressure)
• Kuchuluka kwa malovu (Increased salivation)

Akagwiritsidwa ntchito molakwika kapena mobwerezabwereza, amambitsa: • Dependence (Kudalira mankhwalawo)
• Bladder problems (Mavuto a chikhodzodzo)
• Memory impairment (Mavuto a kukumbukira)

NOTE:
Ketamine si mankhwala obwebwetsa.
Ndi mankhwala abwino akagwilitsidwa ntchito bwino ndi anthu okhawo anazama za mankhwalawa.

💊

ANAESTHETIST SPOTLIGHT GLORIA MPACHIKA LUFESI Behind every safe anaesthesia and successful surgery is a dedicated anaest...
28/07/2026

ANAESTHETIST SPOTLIGHT
GLORIA MPACHIKA LUFESI

Behind every safe anaesthesia and successful surgery is a dedicated anaesthesia provider committed to saving lives.

Meet Gloria Mpachika Lufesi, anaesthesia provider pa Kamuzu Central Hospital (KCH). Amapereka safe anaesthesia kwa odwala opita ku opaleshoni komanso amasamalira odwala kwambiri mu ICU and ma Ermegency.

Gloria amasangalala kwambiri kuphunzitsa Anaesthesia Clinical Officer (ACO) students, pokhulupirira kuti mentoring ndi njira yabwino yolimbikitsira tsogolo la anaesthesia ku Malawi.

Amakhulupirira kuti anaesthesia provider wabwino amaika patient patsogolo, amaganiza mwachangu, amachitapo kanthu pa nthawi yake, ndipo amakhulupirira clinical judgement yake.

Uthenga wawo ndi uwu: "Tiyeni tonse tipereke safe and high quality anaesthesia. Wodwala aliyense amayenera chisamaliro chapamwamba kwambiri."

👏 Zikomo, Gloria, chifukwa cha kudzipereka kwanu pa patient safety, kuphunzitsa atsogoleri am'tsogolo, komanso kulimbikitsa quality ya anaesthesia ku Malawi.



MFUNDO ZITATU ZA ANAESTHESIA: KUCHIZA ULULU (ANALGESIA) Kuchiza ululu ndi imodzi mwa mfundo zitatu zazikulu za anaesthes...
23/07/2026

MFUNDO ZITATU ZA ANAESTHESIA: KUCHIZA ULULU (ANALGESIA)

Kuchiza ululu ndi imodzi mwa mfundo zitatu zazikulu za anaesthesia, pamodzi ndi hypnosis(kugonesa) ndi muscle relaxation(kufewesa/ kumasula minyewa). Kumathandiza wodwala kukhala womasuka komanso kuchira bwino ndi mwansanga

Njira Zochizira Ululu (WHO PAIN MANAGEMENT GUIDELINE )
🟢 Ululu wochepa: Paracetamol, NSAIDs
🟡 Ululu wapakati: Mankhwala ena ophatikizidwa ndi ma opioid ofooka
🔴 Ululu waukulu: Ma opioid amphamvu monga morphine, Pethidine kapena fentanyl moyang'aniridwa bwino.

MULTIMODAL ANALGESIA ndi njira yabwino yomwe anaesthetist amaphatikiza njira zosiyanasiyana zochizira ululu monga mankhwala osiyanasiyana, nerve blocks, ndi regional anaesthesia. Izi zimathandiza kuchepetsa ululu komanso kuchepetsa kugwiritsa ntchito ma opioid ambiri.

⚠️ Ma opioid ndi othandiza koma ayenera kugwiritsidwa ntchito mosamala chifukwa kugwiritsidwa ntchito molakwika kungayambitse kudalira komanso mavuto opuma.

Anaesthetist amazama kwambiri pa kasamalidwe ka ululu, m'chipinda cha opaleshoni, ICU, pa ngozi, ndi m'malo ena osamalira odwala.




BRAVO 👏!!
22/07/2026

BRAVO 👏!!

ONA PANGOLIN  !!DZIWANI ZIPANGIZO ZATHU: LARYNGOSCOPE Munayamba mwadzifunsapo kuti wodwala amapitiriza bwanji kupuma bwi...
22/07/2026

ONA PANGOLIN !!

DZIWANI ZIPANGIZO ZATHU: LARYNGOSCOPE

Munayamba mwadzifunsapo kuti wodwala amapitiriza bwanji kupuma bwino akakhala akugona pa nthawi ya opaleshoni?

Dziwani za laryngoscope — chimodzi mwa zida zofunika kwambiri zomwe anaesthetist amagwiritsa ntchito populumutsa moyo!

Imathandiza anaesthetist kuona bwino mkati mwa mmero kuti athe kuyikamo chubu chopumitsira (breathing tube) mu njira ya mpweya. Izi zimathandiza kuti wodwala apitirize kulandira mpweya wa oxygen pa nthawi ya opaleshoni kapena pakachitika Ermegency

N’chifukwa chiyani ndi yofunika kwambiri?
Chifukwa mpweya uliwonse ndi wofunika.
❌️Popanda njira ya mpweya yotseguka:
❌ Palibe oxygen yokwanira.
❌ Palibe opaleshoni yotetezeka.
❌️palibe Moyo

Ichi ndi chifukwa chake laryngoscope ili pa logo ya Anaesthesia Association of Malawi. Ikuyimira komaso kutikumbusa udindo wathu woteteza njira ya mpweya ya wodwala komanso kupulumutsa miyoyo tsiku lililonse.

Anaesthesia Association of Malawi


KAVALIDWE KOTETEZEKA M'CHIPINDA CHA OPALESHONI (OPERATING THEATRE) Ukatswiri umayambira pa kavalidwe koyenera.Chipinda c...
21/07/2026

KAVALIDWE KOTETEZEKA M'CHIPINDA CHA OPALESHONI (OPERATING THEATRE)

Ukatswiri umayambira pa kavalidwe koyenera.

Chipinda cha opaleshoni chimafuna ukhondo ndi chisamaliro chapamwamba. Kavalidwe koyenera ka ogwira ntchito zaumoyo ndi odwala kamathandiza kupewa matenda komanso kuteteza moyo wa wodwala.

👩🏽‍⚕️ Ogwira ntchito zaumoyo ayenera kuvala:
🟢 Theatre scrubs
🟢 Cap/ Headgear yophimba tsitsi
🟢 Mask yophimba mphuno ndi pakamwa
🟢 Nsapato za theatre
🟢 Eye protection ngati pakufunika
🟢 Sterile gown ndi magolovesi pa ntchito za sterile

👤 Wodwala ayenera:
🟢 Kuvala theatre gown ndi chipewa chophimba tsitsi
🟢 Kuchotsa zodzikongoletsera(ndolo,ring,mano ovekera or zitsulo ), nail polish ndi zinthu zosafunika
🟢 Kukonzedwa mwaukhondo komanso mwaulemu asanachitidwe opaleshoni

🚫 Pewani:
❌ Zodzikongoletsera(ndolo, ring, Necklaces, watch, zibangiri)
❌ Zikhadabo zazitali kapena zopaka polish
❌ Tsitsi kapena ndevu zosaphimbidwa
❌ Kuvala zovala za theatre kunja kwa theatre
❌ Mafuta kapena perfume onunkhira kwambiri

Kumbukirani: Kavalidwe koyenera ndi gawo lofunika pa chitetezo cha odwala, kupewa matenda, ndi opaleshoni yotetezeka.



SURGICAL SAFETY CHECKLIST. Mndandanda wa Chitetezo pa Opaleshoni (Surgical Safety Checklist) ndi chida chosavuta koma ch...
20/07/2026

SURGICAL SAFETY CHECKLIST.

Mndandanda wa Chitetezo pa Opaleshoni (Surgical Safety Checklist) ndi chida chosavuta koma chothandiza kwambiri chomwe chimagwiritsidwa ntchito ndi gulu la anthu ochita opaleshoni pofuna kuonetsetsa chitetezo cha wodwala asanayambe, pa nthawi, komanso pambuyo pa opaleshoni.

Umathandiza kuonetsetsa kuti masitepe ofunikira a chitetezo sakuiwalika ndipo umalimbikitsa kulankhulana momveka bwino komanso kugwirizana pakati pa onse ogwira ntchito m’chipinda cha opaleshoni. Ndipo mndandandawu unagawidwa zigawo zitatu

1.SIGN IN (Asanayambe kupatsa wodwala mankhwala ogonetsa – Anaesthesia)

✅ Tsimikizirani dzina la wodwala.
✅ Tsimikizirani mtundu wa opaleshoni yomwe ichitike.
✅ Tsimikizirani mbali ya thupi yomwe ichitidwe opaleshoni.
✅ Onetsetsani kuti chilolezo cha opaleshoni (consent) chilipo.
✅ Yang'anani makina a anaesthesia ndi mankhwala onse.
✅ Onetsetsani kuti pulse oximeter yalumikizidwa ndipo ikugwira ntchito.
✅ Funsani ngati wodwalayo ali ndi allergy.
✅ Unikani ngati airway(Njira ya mpweya)ingakhale yovuta kapena pali chiopsezo cha aspiration(kusanza).
✅ Unikani ngati pali chiopsezo chotaya magazi ambiri komanso ngati magazi alipo ngati angafunike.

2. TIME OUT (Asanayambe kucheka khungu)

✅ Gulu lonse lidzidziwitse mayina ndi maudindo awo.
✅ Tsimikizirani dzina la wodwala, opaleshoni, ndi malo ochitira opaleshoni.
✅ Dokotala afotokoze zinthu zofunika pa opaleshoniyo.
✅ Wopereka anaesthesia afotokoze mavuto kapena zoopsa zomwe zingachitike.
✅ Namwino atsimikizire kuti zida ndi ukhondo zili bwino.
✅ Tsimikizirani kuti maantibayotiki aperekedwa ngati akufunika.
✅ Onetsetsani kuti zithunzi (X-ray, CT, MRI) zilipo ngati zikufunika.

3. SIGN OUT (Wodwala asanachoke m'chipinda cha opaleshoni)

✅ Tsimikizirani dzina la opaleshoni yomwe yachitika.
✅ Werengani swabs(Thonje,Nsalu,gauze), singano, ndi zida zonse kuti palibe chatsala m'thupi la wodwala.
✅ Lembani bwino ma specimen(nyama) onse.
✅ Nenani ngati panali vuto lililonse la zida.
✅ Gulu lonse likambirane za chisamaliro cha wodwala pambuyo pa opaleshoni (post-operative plan).

NOTE :
"Theatre Checklist imathandiza kuti wodwala azilandira opaleshoni motetezeka, kuchepetsa zolakwika, komanso kupulumutsa miyoyo."



THEATRE NDI IMODZI MWA MALO OTETEZEKA KWAMBIRI KU CHIPATALA.Anthu ambiri amachita mantha akamva kuti akupita ku theatre,...
17/07/2026

THEATRE NDI IMODZI MWA MALO OTETEZEKA KWAMBIRI KU CHIPATALA.

Anthu ambiri amachita mantha akamva kuti akupita ku theatre, koma zoona zake n’zakuti ndi malo amene chitetezo cha wodwala chimaikidwa patsogolo kwambiri.

Mu theatre muli gulu la akatswiri monga anaesthetist, madokotala ochita opaleshoni, anamwino, ndi ogwira ntchito a theatre omwe amagwira ntchito limodzi kuonetsetsa kuti wodwala ali bwino.

Anaesthetist amakhala limodzi ndi wodwala nthawi yonse ya opaleshoni, kuyang’anira kupuma, kugunda kwa mtima, kuthamanga kwa magazi, komanso chitetezo chonse cha wodwala.

🌟 Theatre si malo ochititsa mantha. Ndi malo a chitetezo, mgwirizano, luso, ndi kuchiritsa.

Anaesthesia Association of Malawi ikupitiriza kulimbikitsa:


Address

P. O Box 95
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Anaesthesia Association of Malawi posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share