15/11/2025
DZIWANI IZI
Drug–Food Interactions Amene Anthu Ambiri Amawanyalanyaza .
Pali mankhwala ena amene amagwira ntchito mosiyana kapena kuchepa/kuchuluka mphamvu ngati tamwa limodzi ndi chakudya kapena zakumwa zina. Anthu ambiri samazindikira izi.
1. Mankhwala a BP (ma antihypertensive) + Madzi a Mandimu / Orange / Gr**efruit
Madzi a gr**efruit makamaka amatha kuwonjezera mphamvu ya mankhwala moti munthu angakhale ndi BP yotsika kwambiri kapena zotsatira zoipa zambiri.
Amakhudza mankhwala monga: Amlodipine, Nifedipine, Atorvastatin, Simvastatin.
Chenjezo: Pewani kumwa madzi a gr**efruit mukamamwa mankhwala.
2. Mankhwala a cholesterol (statins) + Madzi a Gr**efruit
Amatha kuwonjezera chiopsezo cha kupweteka kwa minofu kapena kuwonongeka kwa impso.
mankhwala monga artovastatin
3. Antibiotics ena (doxycycline, tetracycline) + Mkaka kapena zinthu za mkaka
Mkaka umachepetsa kulowa m’thupi kwa mankhwala awa.
Zimachepetsa mphamvu yawo pochiza matenda.
Chenjezo: Dikirani osachepera 2 hours musamwe mkaka kapena dikirani 4 hours mutamwa mankhwala.
4. Mankhwala a BP kapena a mtima (ACE inhibitors/spironolactone) + Zakudya zokhala ndi Potassium zambiri
Mbatata, nthochi, avocado, madzi a coconut ali ndi potaziyamu.
Zitha kuwonjezera potaziyamu m’thupi, zomwe zingakhale zowopsa.
5. Warfarin (mankhwala oletsa kuuma kwa magazi) + Zakudya zobiriwira kwambiri
Mbatala, spinach, r**e, broccoli ziyenera kumwedwa m’lingo wokhazikika, osasiyanasiyana kwambiri.
Zakudyazi zili ndi Vitamin K, yemwe amachepetsa mphamvu ya warfarin.
6. Mankhwala a chifuwa/flu okhala ndi caffeine + Khofi kapena energy drinks
Zimatha kuonjezera kusakhazikika kwa mtima, mantha, ndi kugunda mtima mwachangu.
7. Metronidazole + Mowa
Zimakumana ndi kupangitsa:
Kusanza mwamphamvu
Mutu kupweteka,
Kugunda mtima kwambiri
Kutentha thupi
Chenjezo: Pewani mowa masiku 72 mutatha kumwa mankhwala.
8. Mankhwala a mphumu (theophylline) + Khofi / tea / chocolate
Zonsezi zili ndi caffeine ndipo zimatha kuwonjezera zoipa zosatira zakuchuluka caffeine nthupi, kugunda mtima mwachangu, ndi nseru.
9. Mankhwala ochepesa ma acid m'mimba (omeprazole) + Zakudya zamafuta zambiri
Zimachedwetsa kuyamba kugwira ntchito ndipo zimachepetsa mphamvu yake.
Malangizo Ofunika
Nthawi zonse werengani ma instructions a pa botolo la mankhwala.
Funsani wamankhwala (pharmacist ngozo) ngati simukudziwa zakudya zomwe muyenera kupewa.
Osasakaniza mankhwala ndi chakudya mopanda kufunsa akatswiri, makamaka ngati muli ndi matenda aakulu.