02/06/2026
๐AZIBAMBO ZA KUDYA ZANU๐ osachita ulesi welengani.
Azibambo amabiri timadandaula nkhani yoti zikuvuta kudzuka ku bed, komanso ka engine kuchepa tikufuna zokulitsa, Chabwino. Tamverani kaye.
Zonsezi ndizotheka koma ku nkhani yokulitsa kapena kutalikitsa chida ndikuuzani kuti vuto ili limatha kubwela pa zifukwa zosiyanasiyana, mwina kuvulala, kapena kudwalika, kapena nthenda zina za mkati ndipo pena zimangochitika ndithu ndi zina zambiri . Izi ndi chimodzimodzi anthu ena chida chawo ndi cha size yabwino ndithu koma sichimadzuka kwa nthawi yaitali, kapena chimadzuka koma umuna wake owola, kapena wa ngati madzi opanda mphanvu ndipo zotsatira zake za mavuto onsewa munthu wa bambo zinthu ku banja kapena ku chipinda sizimakuyendera. Ndipo mapeto ake mwakangana mwakangananso ndi wa chikondi wanu.
Ngati muli ndi vuto lililonse mwa mavuto awa pitani kaye ku Chipatala tisanagwiritse ntchito ma remedies wa tidziwe kuti kodi vuto mchani. Kenako mkumadya mankhwala.
Mu ndime iyi tiyeni tioneko Zina mwa zakudya zomwe Zingawathandize omwe ali ndi vuto la mphanvu kuchipinda. Chifukwatu enanu omwe muli ndi mavuto tawatchula aja ndinu abwinobwino ndithu Koma vuto ndi zakudya, Zakumwa komanso Zintchito zomwe mmagwira zina ndizoyamwa magazi komanso zokufowoolani mphanvu zanu.
Zakudya izi ndi zomwe zimathandiza kuti mukhale ndi mphavu, Umuna wa mphanvu, komanso kudzuka za mphanvu:
๐-NTHOCHI/Banana:
Mu nthochi muli Enzyme otchedwa bromelain komanso muli Vitamin B6 zomwe zimathandizira kugwira ntchito bwino kwa michere yopangitsa thupi kukhala ready ndi la mphanvu kunkhani ya ku bed.
๐-Pomegranate:
Chipatso ichi ndiye ndichoopsa moti mpaka azungu ena adachipatsa Nickname kuti Superfood for men- Chifukwa choti chimathandizira kuchulutsa chonde mwa azibambo, Chimachulutsa umuna wa mphanvu komanso kupangitsa chida kukhala cha strong.
๐-Mapeyala/ Avocados:
Uyu ndiye tonse tikumudziwa ali ndi Vitamin E, yemwe amathandizanso kupanga Umuna wa mphanvu ndi ochuluka komanso kukupatsa mphanvu mwiniwe.
๐-Ma Grapes:
Ma grapes/Grapes maka aja a black ena amakhala red omapita ku black amakhalanso ndi Resveratrol yemwenso amapanga boost mphanvu za abambo.
๐-Mango/ Ma Oranges/ Mabulosi/ Mandimu:
Zipatso izi zilinso mugulu limeneli, Zili mmaVitamis ngati Vitamin C ndi A zomwenso zimaonjezera mphanvu kwa bambo, Thanzi la ku bed limabwelera. Komanso thupi la munthu limakhala ndi thanzi losakambika.
๐-Nthangala za Maungu:
Izinso ndi dhilu. Madamu wo akaphika maungu onesetsani kuti nthangalazo asataye kapena kugawa kwa ena inu mulipo bambo..zigwileni ntchito ndithu chifukwa zikakuthandizirani penapake kusamala banja.
Machiritso Natural Remedies
๐ฅNgati momwe mwaonelamu zonsezi ndizofunika ndalama. Koma nthawi zina pafunika kumadzisamala ndithu pokonda kudya zimenezi. Ndipo sikuti mukadya pang'ono kapena kamodzi ndiye muona kusintha aayi. Kondani kudya zimenezi daily kaya mukupanga breakfast yanu ikani tina mwa tizipatso timeneti...Pa lunch chimodzimodzi ndipo madzulonso pangani chimodzimodzi.
Izi zidzichitika Everyday ndipo ma results olongosoka mudzayamba kuwaona pakutha kwa mwezi umodzi ena iwiri ndipo ena itatu kumene. Yesetsani mudziphatikiza zipatsozo osati Tsiku ndi tsiku mango okhaokha aayi..
_______________________
Osaiwala kupanga Like...SHARE....FOLLOW